A Prophetic Vision for Malawi

  0
  84

  Zimene Mulungu wandionetsera pa 23 June 2017

  Pa 23 June 2017 nthawi ya 08:45am ndikuganiza zoti ndizuke ndizipita ku bizinesi yanga ndinamva kufooka kwambiri mpaka ndinalephera ku dzuka,sindimadziwa chomwe hinali kuchitika m’moyo mwanga koma ndimanva ngati thupi likupwanya kenako ndinangozindikila kuti ndili mtulo ndipo posakhalitsa ndinamva mau akundiitana koma ndinayangana osamuona munthu amene anali kundiitana ndipo ndinagwidwa ndi mantha kwambiri. Kenako ndinamva kuseka komanso kuchipinda kwanga kunawala mochititsa mantha ndinakuwa kuti anthu andithandize koma palibe anabwera keneko ndinamva mau oti “usaope mwana wanga ndine Mulungu wa mphamvu zonse amene ndinalenga dziko ndi zonse zokhalamo,dzuka uwasatile anthu amene avala zovala zoyelawo ndasankha iwe kuti upulumutse dziko lako mene ndinasankhila yosefe kuti azapulumuse abale ake ku njala”

  Ndinadzidzimuka ndili ndi mantha akulu ndipo ndinangozindikira anthu amene anavala zoyela aja andigwira pa mkono ndipo anali achimwemwe kwambiri andipo anandiuza kuti usaope ife ndife angelo tatumidwa ndi Mlengi.

  Posakhalitsa tinanyamuka koma chodabwitsa timayenda m’malele ndipo tinafika pa malo ena okongola kwambiri kumene kunali mipando ya golide ndipo anandiuza kuti khala pansi usaope,ndimantha ndinakhaladi pansi ndipo anayamba kundifotokozela zamene dziko lathu la Malawi likuyendela

  M’ngelo wina wamaonekedwe okongola kwambiri anayamba kugwetsa mizosi maso mwake ndipo anati ona mwanawe zimene anthu adziko lako akuchita mulungu sali kukondwa nawo.

  Anandionetsa mene anthu timanamizira kupemphera koma kumbari tikuchita zonyasa zambiri,anandionetsa mene anthu sitimakondelana kenako ananditenga kupita pa malo ena kumamene andionetsa zinthu zopatsa mantha kwambiri ndipo ndinafunsa kuti kuno ndikuti ndili ndi mantha akulu. M’ngelo wina anayankha kuti kuno dziko lako la malawi. Ndinafunsa chifukwa sikumaoneka mene timaonela malawiyu kunali ana akhanda koma kumaoneka magazi ochuluka.

  Mwachisoni ndi mantha ndinafunsa kuti kodi ana akhandawa akutani kuno? M’ngelo wina anandiyankha kuti awa ndi ana amene makolo awo anawataya atangobadwa ena asanabadwe nkomwe mai awo anachotsa mimba ndipo misozi ya anawa ikupangitsa kuti makolo awo asapeze mntendele padziko lapansi.
  Kenako anati mulungu sakukondwera ndi mene anthu akupangila chigololo ku malawi atsikana ambiri akumachotsa mimba ndipo enanso akumapha ana awo akabadwa ati kusafuna kukhala ndi ana kuti asawasokoneze zinjoyi zawo.

  Kenako kunabwera m’ngelo wina amene anali wamaonekedwe osiyana ndi anzake onse ndipo anali wachisoni kwambiri ndipo mkanjo wake unali utanyowa kwambiri ndi misozi imene imasika kuchokera maso mwake. “Anati bwera kuno uwone zimene anthu amene amati ndi aneneri komanso otumikira mulungu akumapanga” apapa ndikuti mantha aja atandithera koma ndinali nditazazidwa ndi chisoni kwambiri. Anatenga kachinthu kowala kwambiri kamene kamaoneka ngati limoti ija ya tv kenako anakatobwanya ndipo chomwe chnlinandidabwisa nchakuti atangotobwanya tinapezeka tili pa linthipe bridge pamene anayamba kundionetsa zambiri anati ” wapaona apa,apa ndipamene athu opembeza satana anaikapo ma drum awo kuti pazichitika ngozi koma pano anasamusapo ndikukaika malo ena ” ndinapempha kuti andionetse malo amene akaika ma drum aja koma anakana kuti izi zizachitika pokha pokha anthu atasintha zochita zawo.

  Kenako anatambasula nsalu ina yoyela monyezimila ndipo panali kuoneka ngati kanema posakhalitsa anati waona izi awa ndi anthu amene amati ndi aneneri a mulungu koma ali onyenga ndipo mulungu sakukondwera nawo nkomwe chifukwa akusocheletsa amalawi ambiri.

  Anadiuza kuti ndiwelenge 2 Petulo 2 vesi 1-2.

  Kenako anapitiliza kuti amalawi tikusowa chikondi pakati pathu ndipo izi sizimukondweletsa mulungu chifukwa iye mwini anati chikondi ndiye lamulo lopambana zonse.

  Ndinagwidwa ndimatha akulu pamene anandiuza kuti ngati amalawi sitisintha ndikuyamba kupemphera muchoonadi pa 6 July 2017 kuzachitika ngozi yoopsa kwambiri pamene anthu okwana 150 azataye miyoyo yawo. Ndinafusa kuti nanga mulunguyo walolelanji kuti langa chotere angelo aja anati “mu dziko mukakhala ulamuliro osamvera zofuna za mulungu,iye amalola kuti anthu awonongeke” anatiso mlengi anakupasani wake osankhika pa zisankho za 2014 koma inu munamukana ndipo ndinafusa kuti osankhidwiyo anali ndani koma sanandiuze konse.

  Anandionetsa galimoto ya lorry number plate yake *MJ 4403* imene izapange ngozi ndipo anthu okwana 150 azafa pa 6 July 2017.

  Izi zizachitika pakuti anthu andale ali pakalikiliki othira nsembe kuti azapambane masankho a 2019.

  Original Article

  LEAVE A REPLY

  Please enter your comment!
  Please enter your name here